Dziko la Matamando, Volume I, ndi album yoyimbidwa ndi Congress MusicFactory yomwe imafotokoza za mphamvu ya yosatsutsika ya matamando omwe amakwera kumwamba kuchoka mu community yathu pa dziko lonse lapansi kupita kwa Mfumu yathu ya Ulemelero, Ambuye Mulungu wa Mphamvu zonse!
Mu Dziko la Matamando, Volume I muli nyimbo ngati "Tayima", "Yimba matamando", "Okwezedwa wam’mwamba", "Alinafe", "Kukulambirani Pano ndi Muyaya", "Mwana wa Mulungu", komanso pemphero lolimbikitsa la Dr. Noel Woodroffe "akubwera", kumapeto kwake kunabwerezedwa nyimbo ya “Mwana wa Mulungu".
Imani nafe pamene tikukondwerera ubwino Wake! Fuulani kumwamba pamene tikulengeza kuti ‘Iye ndi Wam’mwamba ndi Wokwezeka’! Imani pamaso pa Mwana wa Mulungu, podziwa kuti Iye ali nafe ndipo Iye akubwera posachedwa!
Nyimbo za matamando zimenezi zochokera ku Congress MusicFactory zikuwonetsa kuyamika, chimwemwe ndi kudzipereka kwa anthu a Mulungu. Ndi chiwonetsero chathu cha kuthokoza kwa Yehova chifukwa cha kupezeka kwake kwakukulu, kukhulupirika komanso chikondi chosalekeza.
Album iyi ndi chiwonetsero champhamvu cha kusiyanasiyana kwa zithu mu Congress WBN komanso kukongola kwa Thupi la Khristu. Kubweretsa pamodzi magulu oimba a pa dziko lonse a Congress MusicFactory, olemba nyimbo, ndi oyimba, album iyi yasonkhanitsa anthu ochokera ku Caribbean, United States, Europe, Africa, Asia, Latin America, ndi Pacific. Iyi ndi album yathu yoyamba mu chiyankhulo cha Chichewa komanso ndi chida cholambilira cha m’mipingo ndi okhulupirira padziko lonse lapansi.
Limbikitsani mzimu wanu, tsitsimutsani moyo wanu ndi kukondwelera chikhulupiliro chanu mu Grace yodabwitsayi, ubwino, ndi ulemerero wa Mfumu yathu Ikudzayo komanso Mulungu Wamuyaya!
Mndandanda wa Nyimbo
- Tayima
- Yimba Matamando
- Okwezedwa Wam’mwamba
- Kukulambirani Pano ndi Muyaya
- Alinafe
- Mwana wa Mulungu
- Akubwera – Mwana wa Mulungu